Yobu 18 BL92

Bilidadi atsutsa Yobu pa kudzikuza kwace, nanena za tsoka la oipa

1 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,

2 Musaka mau kufikira liti?Zindikirani, ndi pamenepo tidzanena.

3 Tiyesedwa bwanji ngati nyama za kuthengo,Ndi kukhala odetsedwa pamaso panu?

4 Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako,Kodi dziko lapansi lisiyidwe cifukwa ca iwe?Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwace?

5 Inde, kuunika kwa woipa kudzazima,Ndi lawi la moto wace silidzawala.

6 Kuunikaku kudzada m'hema mwace,Ndi nyali yace ya pamwamba pace idzazima.

7 Mapondedwe ace amphamvu adzasautsidwa,Ndi uphungu wace wace udzamgwetsa.

8 Pakuti aponyedwa m'ukonde ndi mapazi ace,Namaponda pamatanda.

9 Msampha udzamgwira kucitende,Ndi khwekhwe lidzamkola.

10 Msampha woponda umbisikira pansi,Ndi msampha wa cipeto panjira.

11 Zoopetsa zidzamcititsa mantha monsemo,Nadzampitikitsa kumbuyo kwace.

12 Njala idzatha mphamvu yace,Ndi tsoka lidzamkonzekeratu pambali pace.

13 Zidzatha ziwalo za thupi lace,Mwana woyamba wa imfa adzatha ziwalo zace.

14 Adzazulidwa kuhema kwace kumene anakhulupirira;Nadzatengedwa kumka naye kwa mfumu ya zoopsa.

15 Adzakhala m'hema mwace iwo amene sali ace;Miyala yasulfure idzawazika pokhala pace.

16 Mizu yace idzauma pansi,Ndi nthambi yace idzafota m'mwamba.

17 Cikumbukilo cace cidzatayika m'dziko,Ndipo adzasowa dzina kukhwalala.

18 Adzamkankha acoke ku kuunika alowe kumdima;Adzampitikitsa acoke m'dziko lokhalamo anthu.

19 Sadzakhala naye mwana kapena cidzukulu mwa anthu amtundu wace,Kapena wina wotsalira kumene anakhalako.

20 Akudza m'mbuyo adzadabwa nalo tsiku lace,Monga aja omtsogolera anagwidwa mantha.

21 Zoonadi, zokhalamo osalungama zitero,Ndi malo a iye amene sadziwa Mulungu ndi awa.