Yobu 4 BL92

Elifazi adzudzula Yobu; tsoka la munthu licokera ku zoipa zace; Yobu alape

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2 Munthu akayesa kunena nawe mau, kodi udzamva nao cisoni?Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?

3 Taona iwe walangiza aunyinji,Walimbitsa manja a ofoka.

4 Mau ako anacirikiza iye amene akadagwa,Walimbitsanso maondo otewa.

5 Koma tsopano cakufikira iwe, ndipo ukomoka;Cikukhudza, ndipo ubvutika.

6 Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu,Ndi ciyembekezo cako si ndiwo ungwiro wa njira zako?

7 Takumbukila tsopano, watayika ndani wosaparamula konse?Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?

8 Monga umo ndaonera, olimira mphulupulu,Nabzala bvuto, akololapo zomwezo.

9 Atayika ndi mpweya wa Mulungu,Nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wace.

10 Kubangula kwa mkango, ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,Ndi mano a misona ya mkango atyoledwa.

11 Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,Ndi misona ya mkango waukazi imwazika.

12 Anditengera mau m'tseri,M'khutu mwanga ndinalandira kunong'oneza kwace.

13 M'malingaliro a masomphenya a usiku,Powagwira anthu tulo tatikuru,

14 Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,Nanthunthumira nako mafupa anga onse.

15 Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;Tsitsi la thupi langa lidati nyau nyau.

16 Unaima ciriri, koma sindinatha kuzindikira maonekedwe ace;Panali mzukwa pamaso panga;Kunali cete, ndipo ndidamva mau akuti,

17 Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu?Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wace?

18 Taona, sakhulupirira atumiki ace;Nawanenera amithenga ace zopusa;

19 Kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi,Amene kuzika kwao kuti m'pfumbi,Angothudzulidwa ngati gulugufe,

20 Kuyambira m'mawa kufikira madzulo athudzuka;Aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.

21 Kukometsetsa kwao sikumacotsedwa nao?Amafa koma opanda nzeru.