18 Akali cilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu amuna ndi akazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkuru wao;
19 ndipo taonani, inadza mphepo yaikuru yocokera kucipululu, niomba pa ngondya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
20 Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba maraya ace, nameta mutu wace, nagwa pansi, nalambira,
21 nati, Ndinaturuka m'mimba ya mai wanga wamarisece, wamarisece ndidzanrukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.
22 Mwa ici conse Yobu sanacimwa, kapena kunenera Mulungu colakwa.