7 Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m'dziko ndi kuyendayenda m'mwemo.
8 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.
9 Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu aopa Mulungu pacabe?
10 Kodi simunamcinga iye ndi nyumba yace, ndi zace zonse, pomzinga ponse? nchito ya manja ace mwaidalitsa, ndi zoweta zace zacuruka m'dziko.
11 Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zace zonse, ndipo adzakucitirani mwano pankhope panu.
12 Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Naturuka Satana pamaso pa Yehova.
13 Tsono panali tsiku loti ana ace amuna ndi akazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkuru wao;