1 Pamenepo Yobu anayankha, nati,
2 Zoonadi inu ndinu anthu,Ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.
3 Koma inenso ndiri nayo nzeru monga inu.Sindingakucepereni;Ndani sadziwa zonga izi?
4 Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wace,Ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha;Munthu wolungama wangwiro asekedwa.
5 Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwace,Limlindira woterereka mapazi ace.
6 Mahema a acifwamba akhala mumtendere,Ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima:Amene Mulungu amadzazira dzanja lao.
7 Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza,Ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza;