10 M'dzanja mwace muli mpweya wa zamoyo zonse,Ndi mzimu wa munthu ali yense.
11 M'khutumu simuyesa mau,Monga m'kamwa mulawa cakudya cace?
12 Kwa okalamba kuli nzeru,Ndi kwa a masiku ocuruka luntha.
13 Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu;Uphungu ndi luntha ali nazo.
14 Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso;Amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira,
15 Taona atsekera madzi, naphwa;Awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi.
16 Kwa Iye kuli mphamvu ndi nzeru.Wonyengedwa ndi wonyenga yemwe ali ace.