19 Apita nao, ansembe atawafunkhica,Nagubuduza amphamvu.
20 Amcotsera wokhulupirika kunena kwace.Nalanda luntha la akulu.
21 Atsanulira mnyozo pa akalonga,Nawasezera olimba lamba lao.
22 Abvumbulutsa zozama mumdima,Naturutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera;
23 Acurukitsa amitundu, nawaononganso;Abalalikitsa amitundu, nawabwezanso.
24 Awacotsera akulu a anthu a padziko mtima wao,Nawasokeretsa m'cipululu copanda njira.
25 Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika,Ndipo awayendetsa dzandi dzandi.