5 Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwace,Limlindira woterereka mapazi ace.
6 Mahema a acifwamba akhala mumtendere,Ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima:Amene Mulungu amadzazira dzanja lao.
7 Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza,Ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza;
8 Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza;Ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera,
9 Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse;Kuti dzanja la Yehova licita ici?
10 M'dzanja mwace muli mpweya wa zamoyo zonse,Ndi mzimu wa munthu ali yense.
11 M'khutumu simuyesa mau,Monga m'kamwa mulawa cakudya cace?