9 Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse;Kuti dzanja la Yehova licita ici?
10 M'dzanja mwace muli mpweya wa zamoyo zonse,Ndi mzimu wa munthu ali yense.
11 M'khutumu simuyesa mau,Monga m'kamwa mulawa cakudya cace?
12 Kwa okalamba kuli nzeru,Ndi kwa a masiku ocuruka luntha.
13 Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu;Uphungu ndi luntha ali nazo.
14 Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso;Amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira,
15 Taona atsekera madzi, naphwa;Awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi.