1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,
2 Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika,Ndi kudzaza mimba yace ndi mphepo ya kum'mawa?
3 Kodi atsutsane ndi mnzace ndi mau akusathandiza?Kapena ndi maneno akusaphindulitsa?
4 Zedi uyesa cabe mantha,Nucepsa cilingiriro pamaso pa Mulungu.
5 Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako,Nusankha lilime la ocenjerera.