15 Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ace;Ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pace,
16 Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa,Wakumwa cosalungama ngati madzi.
17 Ndidzakuonetsa, undimvere;Cimene ndinaciona, ndidzakufotokozera;
18 Cimene adacinena anzeru,Adacilandira kwa makolo ao, osacibisa;
19 Ndiwo amene analandira okha dzikoli,Wosapita mlendo pakati pao;
20 Munthu woipa adzipweteka masiku ace onse,Ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa.
21 M'makutu mwace mumveka zoopsetsa;Pali mtendere amfikira wakumuononga.