19 Ndiwo amene analandira okha dzikoli,Wosapita mlendo pakati pao;
20 Munthu woipa adzipweteka masiku ace onse,Ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa.
21 M'makutu mwace mumveka zoopsetsa;Pali mtendere amfikira wakumuononga.
22 Sakhulupirira kuti adzaturukamo mumdima,Koma kuti lupanga limlindira;
23 Ayendayenda ndi kufuna cakudya, nati, Ciri kuti?Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima,
24 Nsautso ndi cipsinjo zimcititsa mantha,Zimlaka ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo;
25 Pakuti amtambasula dzanja lace moyambana ndi Mulungu,Napikisana ndi Wamphamvuyonse.