21 M'makutu mwace mumveka zoopsetsa;Pali mtendere amfikira wakumuononga.
22 Sakhulupirira kuti adzaturukamo mumdima,Koma kuti lupanga limlindira;
23 Ayendayenda ndi kufuna cakudya, nati, Ciri kuti?Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima,
24 Nsautso ndi cipsinjo zimcititsa mantha,Zimlaka ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo;
25 Pakuti amtambasula dzanja lace moyambana ndi Mulungu,Napikisana ndi Wamphamvuyonse.
26 Amthamangira Iye mwaliuma,Ndi zikopa zace zocindikira.
27 Popeza anakuta nkhope yace ndi kunenepa kwace,Nacita mafunyenye a mafuta m'zuuno zace;