32 Cidzacitika isanadze nthawi yace;Pakuti nthambi yace siidzaphuka.
33 Adzayoyoka zipatso zace zosapsa ngati mpesa,Nadzathothoka maluwa ace ngati mtengo wazitona.
34 Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala cumba,Ndi moto udzapsereza mahema a olandira cokometsera mlandu.
35 Aima ndi cobvuta, nabala mphulupulu,Ndi m'mimba mwao mukonzeratu cinyengo.