5 Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako,Nusankha lilime la ocenjerera.
6 Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai.Inde milomo yako ikucitira umboni wakukutsutsa.
7 Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri?
8 Kodi unamva uphungu wacinsinsi wa Mulungu?Ndipo unadzikokera nzeru kodi?
9 Udziwa ciani, osacidziwa ife?Uzindikira ciani, cosakhala mwa ife?
10 Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa,Akuposa atate wako masiku ao,
11 Masangalatso a Mulungu akucepera kodi?Kapena uli naco cinsinsi kodi?