8 Kodi unamva uphungu wacinsinsi wa Mulungu?Ndipo unadzikokera nzeru kodi?
9 Udziwa ciani, osacidziwa ife?Uzindikira ciani, cosakhala mwa ife?
10 Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa,Akuposa atate wako masiku ao,
11 Masangalatso a Mulungu akucepera kodi?Kapena uli naco cinsinsi kodi?
12 Mtima wako usonthokeranji nawe?Maso ako aphethira-phethira cifukwa ninji?
13 Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu,Ndi kulola mau otere aturuke m'kamwa mwako.
14 Munthu nciani kuti akhale woyera,Wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?