2 Zoonadi, ali nane ondiseka;Ndi diso langa liri cipenyere m'kundiwindula kwao.
3 Mupatse cigwiriro tsono, mundikhalire cikole Inu nokha kwanu;Ndani adzapangana nane kundilipirira?
4 Pakuti mwabisira mtima wao nzeru;Cifukwa cace simudzawakuza.
5 Iye wakupereka mabwenzi ace kuukapolo,M'maso mwa ana ace mudzada.
6 Anandiyesanso nthanthi za anthu;Ndipo ndakhala ngati munthu womthira malobvu pankhope pace.
7 M'diso mwanga mucita cizirezire cifukwa ca cisoni,Ndi ziwalo zanga zonse ziribe cithunzi.
8 Anthu oongoka mtima adzadabwa naco,Ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsotsa wonyoza Mulunguyo.