5 Iye wakupereka mabwenzi ace kuukapolo,M'maso mwa ana ace mudzada.
6 Anandiyesanso nthanthi za anthu;Ndipo ndakhala ngati munthu womthira malobvu pankhope pace.
7 M'diso mwanga mucita cizirezire cifukwa ca cisoni,Ndi ziwalo zanga zonse ziribe cithunzi.
8 Anthu oongoka mtima adzadabwa naco,Ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsotsa wonyoza Mulunguyo.
9 Koma wolungama asungitsa njira yace,Ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.
10 Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;Pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.
11 Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,Zace zace zomwe za mtima wanga.