8 Anthu oongoka mtima adzadabwa naco,Ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsotsa wonyoza Mulunguyo.
9 Koma wolungama asungitsa njira yace,Ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.
10 Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;Pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.
11 Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,Zace zace zomwe za mtima wanga.
12 Zisanduliza usiku ukhale usana;Kuunika kuyandikana ndi mdima.
13 Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga;Ndikayala pogona panga mumdima.
14 Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga;Kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga;