5 Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,Ndi kundichulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao;
6 Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,Nandizinga ndi ukonde wace.
7 Taonani, ndipfuula kuti, Ciwawa! koma sandimvera;Ndikuwa, koma palibe ciweruzo.
8 Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,Naika mdima poyendapo ine.
9 Anandibvula ulemerero wanga,Nandicotsera korona pamutu panga,
10 Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu;Nacizula ciyembekezo canga ngati mtengo.
11 Wandiyatsiranso mkwiyo wace,Nandiyesera ngati wina wa adani ace.