1 Koma Yobu anayankha, nati,
2 Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa;Kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwace.
3 Ha! ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu,Kuti ndifike ku mpando wace!
4 Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pace,Ndikadadzaza m'kamwa mwanga ndi matsutsano.
5 Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine,Ndikadazindikira cimene akadanena nane.
6 Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yace yaikuru?Iai, koma akadandicherera khutu.