10 Koma adziwa njira ndilowayi;Atandiyesa ndidzaturuka ngati golidi.
11 Phazi langa lagwiratu moponda Iye,Ndasunga njira yace, wosapambukamo.
12 Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yace;Ndasungitsa mau a pakamwa pace koposa lamulo langa langa.
13 Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani?Ndi ici cimene moyo wace ucifuna acicita.
14 Pakuti adzacita condiikidwiratu;Ndipo zambiri zotere ziri ndi Iye.
15 Cifukwa cace ndiopsedwa pankhope pace;Ndikalingirira, ndicita mantha ndi Iye.
16 Pakuti Mulungu walefula mtima wanga,Ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.