6 Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yace yaikuru?Iai, koma akadandicherera khutu.
7 Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;Ndipo ndikadapulumuka cipulumukire kwa Woweruza wanga.
8 Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye;Kapena m'mbuyo sindimzindikira;
9 Akacita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;Akabisala kulamanja, sindimuona,
10 Koma adziwa njira ndilowayi;Atandiyesa ndidzaturuka ngati golidi.
11 Phazi langa lagwiratu moponda Iye,Ndasunga njira yace, wosapambukamo.
12 Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yace;Ndasungitsa mau a pakamwa pace koposa lamulo langa langa.