11 M'kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta;Aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.
12 M'mudzi waukuru anthu abuula alinkufa;Ndi moyo wa iwo olasidwa upfuula;Koma Mulungu sasamalira coipaco.
13 Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,Sadziwa njira zace,Sasunga mayendedwe ace.
14 Kukaca auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;Ndi usiku asanduka mbala.
15 Ndipo diso la wacigololo liyombekezera cisisira,Ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;Nabvala cophimba pankhope pace.
16 Kuli mdima aboola nyumba,Usana adzitsekera,Osadziwa kuunika.
17 Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa;Pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.