2 Alipo akusendeza malire;Alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.
3 Akankhizira kwao buru wa amasiye,Atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale cikole.
4 Apambukitsa aumphawi m'njira;Osauka a padziko abisala pamodzi.
5 Taonani, ngati mbidzi za m'cipululuAturukira ku nchito zao, nalawirira nkufuna cakudya;Cipululu ciwaonetsera cakudya ca ana ao.
6 Atema dzinthu zao m'munda;Natola khunkha m'munda wampesa wa woipa.
7 Agona amarisece usiku wonse opanda cobvala,Alibe copfunda pacisanu.
8 Abvumbwa ndi mvula kumapiri,Nafukata thanthwe posowa pousapo.