4 Apambukitsa aumphawi m'njira;Osauka a padziko abisala pamodzi.
5 Taonani, ngati mbidzi za m'cipululuAturukira ku nchito zao, nalawirira nkufuna cakudya;Cipululu ciwaonetsera cakudya ca ana ao.
6 Atema dzinthu zao m'munda;Natola khunkha m'munda wampesa wa woipa.
7 Agona amarisece usiku wonse opanda cobvala,Alibe copfunda pacisanu.
8 Abvumbwa ndi mvula kumapiri,Nafukata thanthwe posowa pousapo.
9 Akwatula wamasiye kubere,Natenga cikole cobvala ca osauka;
10 Momwemo ayenda amarisece opanda cobvala,Nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala.