1 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,
2 Kulamulira ndi kuopsa kuti ndi Iye;Acita mtendere pa zam'mwamba zace.
3 Ngati awerengedwa makamu ace?Ndipo ndaniyo, kuunika kwace sikumturukira?
4 Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu?Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?