3 Ngati awerengedwa makamu ace?Ndipo ndaniyo, kuunika kwace sikumturukira?
4 Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu?Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?
5 Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala;Ndi nyenyezi siziyera pamaso pace;
6 Kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi!Ndi wobadwa ndi munthu, ndiyo nyongolotsi!