6 Kumanda kuli padagu pamaso pace,Ndi kucionongeko kusowa cophimbako,
7 Ayala kumpoto popanda kanthu, Nalenjeka dziko pacabe.
8 Amanga madzi m'mitambo yace yocindikira;Ndi mtambo sung'ambika pansi pace,
9 Acingira pa mpando wace wacifumu,Nayalapo mtambo wace.
10 Analembera madziwo malire,Mpaka polekeza kuunika ndi mdima.
11 Mizati ya thambo injenjemera,Ndi kudabwa pa kudzudzula kwace.
12 Mwa mphamvu yace agwetsa nyanja bata;Ndipo mwa luntha lace akantha kudzikuza kwace.