3 Pakuti moyo wanga wonse ukali mwa ine,Ndi mpweya wa Mulungu m'mphuno mwanga;
4 Milomo yanga siilankhula cosalungama,Ndi lilime langa silichula zacinyengo.
5 Sindibvomereza konse kuti muli olungama;Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.
6 Ndiumirira cilungamo canga, osacileka;Cikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.
7 Mdani wanga akhale ngati woipa,Ndi iye amene andiukira ngati wosalungama.
8 Pakuti ciyembekezo ca wonyoza Mulungu nciani pomlikhatu Mulungu,Pomcotsera moyo wace?
9 Kodi Mulungu adzamvera kupfuula kwace, ikamdzera nsautso?