5 Sindibvomereza konse kuti muli olungama;Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.
6 Ndiumirira cilungamo canga, osacileka;Cikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.
7 Mdani wanga akhale ngati woipa,Ndi iye amene andiukira ngati wosalungama.
8 Pakuti ciyembekezo ca wonyoza Mulungu nciani pomlikhatu Mulungu,Pomcotsera moyo wace?
9 Kodi Mulungu adzamvera kupfuula kwace, ikamdzera nsautso?
10 Kodi adzadzikondweretsa naze Wamphamvuyonse,Ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse?
11 Ndidzakulangizani za dzanja la Mulungu;Cokhala ndi Wamphamvuyonse sindidzacibisa.