9 Kodi Mulungu adzamvera kupfuula kwace, ikamdzera nsautso?
10 Kodi adzadzikondweretsa naze Wamphamvuyonse,Ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse?
11 Ndidzakulangizani za dzanja la Mulungu;Cokhala ndi Wamphamvuyonse sindidzacibisa.
12 Taonani, inu nonse munaciona;Ndipo mugwidwa nazo zopanda pace cifukwa ninji?
13 Ili ndi gawo la munthu woipa kwa Mulungu,Ndi colowa ca akupsinja anzao acilandira kwa Wamphamvtiyonse.
14 Akacuruka ana ace, ndiko kucurukira lupanga,Ndi ana ace sadzakhuta cakudya.
15 Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa,Ndi akazi ace amasiye sadzalira maliro.