2 Citsulo acitenga m'nthaka,Ndi mkuwa ausungunula kumwala.
3 Munthu athawitsa mdima,Nafunafuna mpaka malekezero onse,Miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.
4 Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu;Aiwalika ndi phazi lopitapo;Apacikika kutali ndi anthu, nalendewa-lendewa.
5 Kunena za nthaka, kucokera momwemo mumaturuka cakudya,Ndi m'munsi mwace musandulizika ngati ndi moto.
6 Miyala yace ndiyo malo a safiro,Ndipo iri nalo pfumbi lagolidi.
7 Njira imeneyi palibe ciombankhanga ciidziwa;Lingakhale diso la kabawi losapenyapo.
8 Nyama zodzikuza sizinapondapo,Ngakhale mkango waukali sunapitapo.