17 Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine,Ndi zowawa zondikungudza sizipuma.
18 Mwa mphamvu yaikuru ya nthenda yanga cobvala canga cinasandulika,Cindithina ngati pakhosi pa maraya anga.
19 Iye anandiponya m'matope,Ndipo ndafanana ndi pfumbi ndi phulusa.
20 Ndipfuula kwa Inu, koma simundiyankha;Ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera.
21 Mwasandulika kundicitira nkharwe;Ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.
22 Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo;Ndipo mundisungunula mumkuntho.
23 Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa,Ndi ku nyumba yokomanamo amoyo onse.