19 Iye anandiponya m'matope,Ndipo ndafanana ndi pfumbi ndi phulusa.
20 Ndipfuula kwa Inu, koma simundiyankha;Ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera.
21 Mwasandulika kundicitira nkharwe;Ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.
22 Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo;Ndipo mundisungunula mumkuntho.
23 Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa,Ndi ku nyumba yokomanamo amoyo onse.
24 Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lace kodi?Akati aonongeke, sapfuulako kodi?
25 Kodi sindinamlirira misozi wakulawa zowawa?Kodi moyo wanga sunacitira cisoni osowa?