23 Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa,Ndi ku nyumba yokomanamo amoyo onse.
24 Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lace kodi?Akati aonongeke, sapfuulako kodi?
25 Kodi sindinamlirira misozi wakulawa zowawa?Kodi moyo wanga sunacitira cisoni osowa?
26 Muja ndinayembekeza cokoma cinadza coipa,Ndipo polindira kuunika unadza mdima.
27 M'kati mwanga mupweteka mosapuma,Masiku a mazunzo andidzera.
28 Ndiyenda ndiri wothimbirira osati ndi dzuwa ai;Ndinyamuka mumsonkhano ndi kupfuula,
29 Ndiri mbale wao wa ankhandwe,Ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.