26 Muja ndinayembekeza cokoma cinadza coipa,Ndipo polindira kuunika unadza mdima.
27 M'kati mwanga mupweteka mosapuma,Masiku a mazunzo andidzera.
28 Ndiyenda ndiri wothimbirira osati ndi dzuwa ai;Ndinyamuka mumsonkhano ndi kupfuula,
29 Ndiri mbale wao wa ankhandwe,Ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.
30 Khungu langa lada, nilindipfundukira;Ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.