5 Anawapitikitsa pakati pa anthu,Awapfuulira ngati kutsata mbala.
6 Azikhala m'zigwa za cizirezire,M'maenje a m'nthaka ndi m'mapanga.
7 Pakati pa zitsamba alira ngati buru,Pansi pa khwisa asonkhana pamodzi.
8 Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina;Anawaingitsa kuwacotsa m'dziko.
9 Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo,Nandiyesa nthanthi.
10 Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine,Saleka kuthira malobvu pankhope panga.
11 Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza;Anataya comangira m'kamwa mwao pamaso panga.