8 Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina;Anawaingitsa kuwacotsa m'dziko.
9 Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo,Nandiyesa nthanthi.
10 Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine,Saleka kuthira malobvu pankhope panga.
11 Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza;Anataya comangira m'kamwa mwao pamaso panga.
12 Ku dzanja langa lamanja anauka oluluka,Akankha mapazi anga,Andiundira njira zao zakundiononga.
13 Aipsa njira yanga,Athandizana ndi tsoka langa;Ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi.
14 Akudza ngati opitira pogamuka linga papakuru,Pakati pa zopasuka adzigubuduza kundidzera ine.