15 Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenga iyenso?Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?
16 Ngati ndakaniza aumphawi cifuniro cao,Kapena kutopetsa maso a amasiye,
17 Kapena kudya nthongo yanga ndekha,Osadyako mwana wamasiye;
18 (Pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate;Ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye cibadwire ine.)
19 Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda cobvala,Kapena kuti wosowa alibe copfunda;
20 Ngati zuuno zace sizinandiyamika,Ngati sanapfunda ubweya wa nkhosa zanga;
21 Ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa,Popeza ndinaona thandizo langa kucipata;