17 Kapena kudya nthongo yanga ndekha,Osadyako mwana wamasiye;
18 (Pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate;Ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye cibadwire ine.)
19 Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda cobvala,Kapena kuti wosowa alibe copfunda;
20 Ngati zuuno zace sizinandiyamika,Ngati sanapfunda ubweya wa nkhosa zanga;
21 Ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa,Popeza ndinaona thandizo langa kucipata;
22 Libanthuke phewa langa paphalo,Ndi dzanja langa liduke pagwangwa.
23 Pakuti tsoka locokera kwa Mulungu linandiopsa,Ndi cifukwa ca ukulu wace sindinakhoza kanthu,