2 Pakuti gawo la Mulungu locokera kumwamba,Ndi colowa ca Wamphamvuyonse cocokera m'mwambamo nciani?
3 Si ndizo cionongeko ca wosalungama,Ndi tsoka la ocita mphulupulu?
4 Nanga sapenyanjira zanga,Ndi kuwerenga moponda mwanga monse?
5 Ngati ndinayanjana nalo bodza,Ndi phazi langa linathamangira cinyengo;
6 Andiyese ndi muyeso wolingana,Kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga.
7 Ngati phazi langa linapambuka m'njira,Ndi mtima wanga unatsata maso anga?Ngati cirema camamatira manja anga?
8 Ndibzale ine nadye wina,Ndi zondimerera ine zizulidwe.