6 Andiyese ndi muyeso wolingana,Kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga.
7 Ngati phazi langa linapambuka m'njira,Ndi mtima wanga unatsata maso anga?Ngati cirema camamatira manja anga?
8 Ndibzale ine nadye wina,Ndi zondimerera ine zizulidwe.
9 Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,Ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,
10 Mkazi wanga aperere wina;Wina namuike kumbuyo.
11 Pakuti ico ndi coipitsitsa,Ndico mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wace.
12 Pakuti ndico moto wakunyeka mpaka cionongeko,Ndi cakuzula zipatso zanga zonse.