11 Pakuti ambwezera munthu monga mwa nchito yace,Napezetsa munthu ali yense monga mwa mayendedwe ace.
12 Ndithu zoonadi, Mulungu sangacite coipa,Ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.
13 Anamuikiza dziko lapansi ndani?Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani?
14 Akadzikumbukila yekha mumtima mwace,Akadzisonkhanitsira yekha mzimu wace ndi mpweya wace,
15 Zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi,Ndi munthu adzabwerera kupfumbi.
16 Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ici,Cherera khutu kunena kwanga.
17 Kodi munthu woipidwa naco ciweruzo adzalamulira?Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?