15 Zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi,Ndi munthu adzabwerera kupfumbi.
16 Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ici,Cherera khutu kunena kwanga.
17 Kodi munthu woipidwa naco ciweruzo adzalamulira?Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?
18 Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pace iwe,Kapena kwa akalonga, Oipa inu?
19 Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga,Wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka?Pakuti onsewo ndiwo nchito ya manja ace.
20 M'kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku,Anthu agwedezeka, napita,Amphamvu acotsedwa opanda dzanja lakuwacotsa.
21 Pakuti maso ace ali pa njira ya munthu ali yense,Napenya moponda mwace monse.