2 Tamverani mau anga, inu anzeru;Mundicherere khutu inu akudziwa.
3 Pakuti khutu liyesa mau,Monga m'kamwa mulawa cakudya.
4 Tidzisankhire coyeneraco,Tidziwe mwa tokha cokomaco.
5 Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama,Ndipo Mulungu wandicotsera coyenera ine.
6 Kodi ndidzinamizire?Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwa.
7 Wakunga Yobu ndani,Wakumwa mwano ngati madzi?
8 Wakutsagana nao ocita mphulupulu,Nayendayenda nao anthu oipa.