22 Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa,Kuti ocita zopanda pace abisaleko.
23 Pakuti Mulungu alibe cifukwa ca kulingiriranso za munthu,Kuti afike kwa. Iye kudzaweruzidwa.
24 Aphwanya eni mphamvu osaturutsa kubwalo mlandu wao,Naika ena m'malo mwao.
25 Pakuti asamalira nchito zao,Nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.
26 Awakantha ngati oipa,Poyera pamaso pa anthu.
27 Popeza anapambuka, naleka kumtsata,Osasamalira njira zace ziri zonse.
28 M'mwemo anafikitsa kwa Iye kupfuula kwa osauka;Ndipo anamva Iye kupfuula kwa ozunzika.