26 Awakantha ngati oipa,Poyera pamaso pa anthu.
27 Popeza anapambuka, naleka kumtsata,Osasamalira njira zace ziri zonse.
28 M'mwemo anafikitsa kwa Iye kupfuula kwa osauka;Ndipo anamva Iye kupfuula kwa ozunzika.
29 Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani?Akabisa nkhope yace adzampenyerera ndani?Cikacitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, ncimodzimodzi;
30 Kuti munthu wonyoza Mulungu asacite ufumu,Ndi anthu asakodwe mumsampha,
31 Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu,Ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwa?
32 Cimene sindiciona mundilangize ndi Inu,Ngati ndacita cosalungama sindidzabwerezanso.