4 Tidzisankhire coyeneraco,Tidziwe mwa tokha cokomaco.
5 Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama,Ndipo Mulungu wandicotsera coyenera ine.
6 Kodi ndidzinamizire?Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwa.
7 Wakunga Yobu ndani,Wakumwa mwano ngati madzi?
8 Wakutsagana nao ocita mphulupulu,Nayendayenda nao anthu oipa.
9 Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nakoKubvomerezana naye Mulu ngu.
10 Cifukwa cace mundimvere ine, eni nzeru inu,Nkutali ndi Mulungu kucita coipa,Ndi Wamphamvuyonse kucita cosalungama.