1 Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,
2 Kodi muciyesa coyenera,Umo mukuti, Cilungamo canga ciposa ca Mulungu,
3 Pakuti munena, Upindulanji naco?Posacimwa ndinapindula ciani cimene sindikadapindula pocimwa?
4 Ndidzakuyankhani,Ndi anzanu pamodzi ndi inu.
5 Yang'anani kumwamba, nimuone,Tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.
6 Ngati mwacimwa, mumcitira Iye ciani?Zikacuruka zolakwa zanu, mumcitira Iye ciani?
7 Mukakhala wolungama, mumninkhapo ciani?Kapena alandira ciani pa dzanja lanu?